"ANYAMATA AKUNDIONETSA ZABWINO" - KAJAWA
Mphunzitsi watsopano kutimu ya Bangwe All Stars, Trevor Kajawa, wati osewera timuyi akuoneka kuti akulimbikira kwambiri kuti amuonetse kuthekera kwawo zomwe zikupereka chilimbikitso kuti lero akachita bwino.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero ake oyamba kutimuyi pomwe akukumana ndi timu ya Mighty Mukuru Wanderers mu chikho cha Airtel Top 8 ndipo wati anyamata akufuna kuyiwala za kale ndikuyang'ana kutsogolo.
"Akhala masewero ovuta kwambiri koma ndi 50-50 poti ndi chikho nde tikalimbikira. Anyamata akundionetsa zinthu zapamwamba kwambiri mwina akufuna ndione mmene angapangire nde ngati akagwiritse ntchito zomwe tapanga pokonzekera ndekuti zitha kukatiyendera bwino." Anatero Kajawa.
Iye anati timu yake ikufunitsitsa ikakane kugonja pa masewero amenewa cholinga akadzabwera pakhomo pawo adzachite bwino.
Timuyi inakwanitsa kumaliza pa nambala yachisanu ndi chimodzi mu ligi ya chaka chatha yomwe inali yoyamba kwa iwo koma chaka chino avutika k
Noma ikuwina osati zmenez ayi
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores