2
WIN 2
"KUIMA KWA LIGI KUSOKONEZA MATIMU ENA" - MITAMBO
Katswiri wozukuta nkhani zamasewero mdziko muno, Justice Mitambo, wati kuima kwa masewero kwa masabata pafupifupi atatu kukhudza matimu amu TNM Supa ligi pomwe omwe amachita bwino akhonza kulowa pansi.
Iye amayankhula patsogolo pa kuyambiranso kwa masewero mdziko muno atayima kamba koti Flames imasewera masewero opitira ku World Cup ya 2026 komanso polira maliro a anthu asanu ndi atatu omwe anamwalira pa ngozi ya ndege.
Iye wati molalo ya matimu omwe amachita bwino ngati Silver Strikers, Mzuzu City Hammers komanso Kamuzu Barracks itha kulowa pansi pomwe ena atha kukonzanso zolakwika zawo.
"Molalo omwe unalipo kwa matimu omwe anayaka moto tisanapite ku tchuthi sungakhale chimodzimodzi pokhapokha aphunzitsi komanso akuluakulu awalimbikitse. Tinaona Silver Strikers itagonjetsa Jenda United ikuchokera kogonjetsa FCB Nyasa Big Bullets molalo umenewu utha kukhala pano wazizira."
"Matimu ngati Mzuzu City Hammers komanso Kamuzu Barracks san