"TIKUFUNIKA KUKONZA KUMBALI YOGOLETSA" - BUNYA
Mphunzitsi watimu ya Dedza Dynamos, Andrew Bunya, wati timu yake ili ndi ntchito yokonza kutsogolo kwawo ngati akufunikira kuti ayambe kupezanso zipambano mu ligi ya TNM.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi MAFCO pa bwalo la Dedza lamulungu ndipotu wati anyamata ake akusewera bwino ndipo akangokwanitsa kumagoletsa ndekuti zipambano ziwapeza.
"Masewero apita aja mipata tinayipeza yochuluka kwambiri koma kuti tigoletse kukanika, timatha kupita kutsogolo komanso kupangitsa kuti anzathu alakwitse kumbuyo kwawo koma kuti mpira ugunde ukonde ukamanika nde tikonza mbali imeneyo zimatheka tiyambanso kuchita bwino." Anatero Bunya.
Timuyi ikupita mmasewerowa ikusaka chipambano chawo choyamba pomwe yagonja kamodzi ndi kufanana mphamvu katatu kuti akhale ndi mapointsi atatu pa masewero anayi pa nambala 12.
Live tiwina yomweyo
Prediction 2-0 prediction
Prediction 1 - 0 prediction💯
Prediction 1-0
Prediction Kamuzu 1 Bangwe 0