THOM WAPITA KU TP MAZEMBE
Katswiri wa Scorchers, Sabina Thom, atumikira timu ya amayi osewera mpira wamiyendo ya TP Mazembe yaku DRC pomwe wasaina mgwirizano wa zaka ziwiri ndi timuyi.
Katswiriyu anachoka sabata yatha kupita kutimuyi komwe amakayesetsa zachipatala ndipo wakhonza komanso timu yake ya MDF Lionesses yatsimikiza za nkhaniyi. Poyankhula ndi Thom, iye wati ndi okondwa kupita ku timuyi.
"Ndi zokoma kwambiri ndipo ndine osangalala kukhala mbali imodzi ya timu ngati iyiyi ndipo anali maloto anga kutumikira timu yaikulu ngati TP Mazembe." Anafotokozapo Thom.
Katswiriyu wakhala ofunikira kumbali ya Scorchers pomwe anaithandiza kufika mu ndime yotsiriza mu mpikisano wa COSAFA Women's Championship. Iye amasewera pakati chakumanja kapenanso kutsogolo ndipo ndi msilikali wa dziko lino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores