Katswiri wakale wa FCB Nyasa Big Bullets, Chimwemwe Idana, akhalabe kutimu ya Silver Strikers kutsatira kulengeza kwa timuyi kuti katswiriyu amaliza ligi ya chaka chino.
Timu ya Silver Strikers yalengeza usiku wa lachisanu mothokoza akuluakulu a timuyi pokambirana ndi timu ya Mbeya City zotenga katswiriyu.
Idana wakhala wofunikira kutimuyi pomwe wagoletsa zigoli zinayi ndikuthandizira zina zisanu ndi chimodzi (6).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores