SILVER YATI IDANA SAKUCHOKA
Timu ya Silver Strikers yatsutsa mphekesera zomwe zayenda pa tsamba la mchezo kuti katswiri wawo, Chimwemwe Idana, akuchoka kutimuyi pomwe yati anthu akumafalitsa nkhani zambiri zabodza.
Oyankhulira timuyi, Peter Masiye, wati akudabwa ndi zimene anthu akunenazi ndipo timuyi ikhale ndi Idana mpaka kumapeto kwa ligi ya chaka chino.
"Mgwirizano wa ife ndi Idana ukadalipo ndipo tangodabwa nazo nkhani zimenezi koma ndikufuna nditsimikizire onse otsatira ma Banker kuti Idana ndi wathu ndipo timaliza naye chaka chino." Anatero Masiye.
Idana anapita kutimuyi pangongole kuchokera ku timu ya Mbeya FC yaku Tanzania ndipo Silver inalengeza mu June kuti osewerayu akhalebe kutimuyi koma sanafotokoze mgwirizano weniweni pa katswiriyu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores