"TIMAKONZA TSOPANO TIKOLOLE" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, wati timu yake tsopano ili bwino ndipo tsopano iyambe kukolola zomwe amafesa mchigawo choyamba.
Nyambose amayankhula izi atatha masewero omwe timu yake inalepherana 1-1 ndi FCB Nyasa Big Bullets pa bwalo la Kamuzu lachitatu. Iye anali osangalala ndi kaseweredwe katimuyi ndipo wati mchigawo chachiwiri, iwo agwira ntchito yaikulu.
"Timu yathu sinatuluke koma kungoti kubwera kwa osewera atsopano ku timuyi kunapangitsa kuti zina zizivuta koma tsopano takonza ndipo taona kusintha lero tagoletsa chigoli chabwinobwino pomwe ndi Blue Eagles timaphonya kwambiri apa tiyamba kukolola zomwe timalima." Anatero Nyambose.
Iye anatinso ndi okondwa poti timu yake sikuchinyitsa kwambiri pomwe wati ndi Chitipa yokha yomwe inagoletsa zigoli ziwiri pa iwo. Timuyi yamaliza pa nambala 14 ndi mapointsi 14 mu chigawo choyamba.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores