IDANA WAPITA KU ZAMBIA
Katswiri wa Flames, Chimwemwe Idana, wafika mdziko la Zambia komwe zamveka kuti apita kutimu ya Kabwe Warriors ya mdzikomo.
Idana anatumikira timu ya Silver Strikers mchigawo choyamba cha ligi ya chaka chino koma mgwirizano wake wa pangongole kuchokera ku timu ya Mbeya City ndi Silver unatha.
Silver yakanika kugula katswiriyu kamba koti matimuwa sanamvane mtengo ndipo Mbeya ikutumizanso katswiriyu pa ngongole.
Tsatanetsatane wa nkhaniyi tikhale tikukupatsirani mu nkhani zathu zotsatira.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores