IDANA AKHONZA KUBWERERA KU SILVER
Katswiri wa timu ya Flames, Chimwemwe Idana, akhonza kubwereranso kutimu ya Silver Strikers pomwe akulingalira zothetsa mgwirizano wake ndi timu ya Mbeya City.
Izi ndi malingana ndi malipoti a nyuzipepala ya Times yomwe yalemba kuti katswiriyu akufuna kuthetsa mgwirizanowu pomwe akulephera kupeza timu yosewerako mu ma ligi a chaka chino.
Idana ali mdziko la Zambia pomwe amafuna kupita ku imodzi mwa matimu atatu omwe amamufuna koma mpaka pano palibe chachitika. Timu ya Mbeya ikufuna K24 million pa Idana kapena katswiriyu akasewerere timuyi yomwe inatuluka mu ligi yaikulu koma iye akukana.
Ndipo Owinna ili ndi malipoti oti Idana akhonza kupita ku Silver mwaulere akathetsa mgwirizano wake.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores