"OSEWERA TAGWIRIZANA KUTI TITENGE COSAFA" - CHAWINGA
Mtsogoleri wa timu ya Scorchers ku mpikisano wa COSAFA Women's Championship, Temwa Chawinga, wati iye ndi timu yake agwirizana kuti chaka chino chokha atengeko chikhochi koyamba mu mbiri ya mpira.
Chawinga amayankhula izi patsogolo pa masewero awo ndi Mozambique mu ndime ya matimu anayi a chikhochi lachisanu ndipo wati timu yawo ndi yokonzeka kupanga chilichonse kuti akhale ukatswiri.
"Zokonzekera zikuyenda bwino atsikana tonse mu camp molalo ili pa mwamba pomwe tikupita mmasewerowa. Tinayamba kusewera mpikisanowu ndi kalekale ndipo tagwirizana kuti mwina chaka chino titengeko." Anatero Chawinga.
Iye anatinso masewero awo ndi Mozambique akhala ovuta potengera kuti matimu ambiri abwera mwa mphamvu ndipo samayembekezera timuyi kufika mu ndimeyi nde chizolowezi choti amayigonjetsa sichigwira.
Malawi ikumana ndi Mozambique mawa pomwe akufuna kufika ndime yotsiriza kachiwiri mu zaka zitatu. Matimu a Zambia ndi Zimbabwe akumananso mma
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores