"MWAYI UKADALIPO OTSALA MU LIGI" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watimu ya Red Lions, Malumbo Mkandawire, wati timu yake iyesetsabe kumenyera nkhondo mmasewero omwe atsala nawo kuti mwina asatuluke mu ligi pomwe wati mwayi akadali nawo.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe afanana mphamvu ndi Civo United 0-0 pa bwalo la Civo ndipo wati ndi wokhutira ndi zotsatirazi zomwe zithandize timu yawo.
"Poti tinali koyenda, point ndi yabwino ndipo ndasangalala nayo pomwe sitinagonje. Mwayi ukadalipo ndipo tikhala tikuyesabe kuti mwina tisatuluke koma mwayi ulipobe." Anatero Mkandawire.
Red Lions yatsala ndi masewero anayi ndipo akuyenera kupambana mmasewero onse kuti mwina angatsale mu ligiyi pomwe ali ndi mapointsi 22 pa masewero 26 pa nambala 15.
#KasongaJr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores