"TIKHONZA KUTSALIRABE MU LIGI" - MASAPULA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Red Lions, Chifundo Masapula, wati timu yake tsopano ili ndi mwayi oti itha kutsala mu ligi pomwe tsopano akufunikira kuchita bwino mmasewero awo.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe timuyi yagonjetsa Extreme FC 2-1 pa bwalo la Balaka ndipo wati mmene anyamata ake akuchitira, akupereka chilimbikitso kuti atsala mu ligi.
"Kukonzekera kwathu kunali kwa pamwamba chifukwa timadziwa kuti masewero alero ndi apampeni koma tithokoze kuti tawina. Mwayi ulipo wochuluka, anyamata akuonetsa kuti ali tsopano bwino koma asamasuke kuti alibwino chifukwa zikhonza kuwasokonekera." Anatero Masapula.
Timuyi ili pa nambala 15 mu ligi ndipo yatsala ndi masewero okwana atatu kuti imalize ligi ndipo ikufunikira mapointsi anayi kuti ichoke ku chigwa cha matimu otuluka ndipo ili ndi mapointsi 25.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores