GULU LA MANOMA LAPEREKA NDALAMA KU BANJA LA LEMIAS JESTER
Gulu lapa WhatsApp la masapota a Mighty Mukuru Wanderers lotchedwa Mighty Wanderers Fan base lapereka ndalama yokwana K300,000 ku banja la a Lemias Jester omwe anamwalira mu chaka cha 2013.
A Jester anamwalira kutsatira zipolowe zomwe zinabuka pa masewero omwe timuyi inkasewera ndi Silver Strikers pa bwalo la Balaka ndipo anamwalilira pa bwalo lomweli.
Mmodzi mwa oyendetsa gululi, Trinity Chisanu, wati iwo anapita ku Ntcheu pofuna kuonetsa banjali kuti akadali nawo limodzi.
"Titaona kuti tikulowa mu chaka china, tinafuna kusangalala ndi banjali ndikuwaonetsa kuti timawakumbukirabe." Anatero Chisanu.
Ndipo polandira ndalamayo, mkazi wa malemuwa wathokoza gululi kamba ka thandizoli limene liwathandize pa mavuto ena omwe akumakumana nawo pakhomoli.
Gululi lili ndi anthu okwana 96 ndipo ndi omwe anagwirizana ndi kusonkha ndalamazi ngati mbali imodzi yothandiza kudzera mu timu yawoyi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr