BABATUNDE SAPEZEKA NDI MOYALE
Katswiri wa timu ya FCB Nyasa Big Bullets, Babatunde Adepoju, sapezeka pa masewero omwe timuyi isewere ndi Moyale Barracks mu ligi lamulungu kamba koti ali ndi makadi achikasu atatu.
Izi zadziwika malingana ndi ndandanda wa osewera omwe sapezeka sabata ino kamba ka makadi womwe Super League of Malawi yatulutsa.
Katswiriyu wakhala wofunikira kutimuyi pomwe wagoletsa zigoli zisanu mmasewero asanu apitawa atimuyi mu mipikisano yonse kuphatikiza zigoli ziwiri ziwiri pa Blantyre Derby.
Enanso mwa osewera omwe sapezeka sabata ino ndi Osman Ackim, Josiah Duwa ndi Ojumu Gbolahani a Bangwe All Stars, Raphael Phiri wa Moyale ndi Peter Kasonga wa MAFCO.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr π·: Bullets media
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores