BANGWE YATENGA KAJAWA
Timu ya Bangwe All Stars yalemba ntchito Trevor Kajawa ngati mphunzitsi wawo wamkulu kutsatira kuchoka kwa Rodgers Yasin kamba kosachita kwa timuyi.
Timuyi yatsimikiza nkhaniyi pa tsamba lawo la Facebook ndipo yati ikuyembekeza zabwino kuchokera kwa mphunzitsi wakale wa Tigers komanso Karonga United.
Ndipo katswiri wakale wa Mighty Mukuru Wanderers, Alfred Manyozo akhale wachiwiri wake ndipo Owen Chaima akhale mphunzitsi wa otchinga pagolo.
Kajawa ndi mphunzitsi wachinayi kuphunzitsa timuyi kutsatira kupezeka kwa Christopher Nyambose, Mapopa Msukwa komanso Yasin mu chaka chino chokha.
Bangwe ili pa nambala 15 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 12 pa masewero 19 omwe yasewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores