"BULLETS NDI TIMU YABWINO KOMA SICHIOPSEZO KWA IFE" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Trevor Kajawa, wati masewero atimu yake ndi FCB Nyasa Big Bullets atha kukhala chiyambi cha zinthu zabwino pomwe ngati angapeze zotsatira zabwino akhale akusintha pa mapointsi awo.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aseweredwe pa bwalo la Kamuzu lachinayi ndipo wati timu yake yakonzeka bwino kuti mwina ichite bwino.
"Akhala masewero ovuta kwambiri poti Bullets ndi timu yabwino kwambiri koma sichiopsezo kwa Ife, kutengera pomwe Ife tili paja ndi poyipa nde tikufunikira kuti tiyambe kutolera mapointsi kuti tiyambe kusuntha nde masewero awa atha kukhala chiyambi cha zabwino." Anatero Kajawa.
Iye anati masewero omwe anagonja 1-0 ndi Mighty Mukuru Wanderers mu chikho cha Airtel Top 8 ndi osiyana ndi a lero poti zolinga zinali zosiyana kwambiri ndipo lero ayesetsa kuti apambane.
Timuyi ili pa nambala 15 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana 12 ndipo akusiyana mapointsi asanu nd
Bullets 2 : 1 Bangwe ๐ฅ๐ฅ๐ฅ
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores