"TIYENERA KUTI TIYAMBE KUKWERA MMWAMBA" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Trevor Kajawa, wati timu yake ikuyenera kupambana mtsiku la lero kuti iyambe kupita pamwamba mu ligi cholinga choti asatuluke mu ligi ya TNM.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi timu ya Baka City pa bwalo la Balaka lero ndipo wati anayiwala za chipambano chawo ndi FCB Nyasa Big Bullets tsopano akuyang'ana mwachidwi masewero awo ndi Baka.
"Anyamata ali chimodzimodzi mmene analili koma masewero a Bullets tinawayiwala padakali panopa tikupanga za Baka ndipo anyamata akuzindikira kuti sali malo abwino koma kuti asuntheko nde tikuyenera kuti tipambane." Anatero Kajawa.
Iye wati masewero omwe timu yake ikuyenera kudalira kuti izipita kutsogolo ndi monga amenewa ndipo mwanjira iliyonse akuyenera kuti apambane.
Timuyi ili pa nambala 15 mu ligi ndi mapointsi okwananso 15 pa masewero 20 omwe yasewera ndipo ikapambana iyandikira FOMO FC yomwe ili kunja kwa chigwa cha matimu otuluka mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores