"TIKAYESETSA KUTI TIKAWINE" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Trevor Kajawa, wati akayesetsa kuti apeze chipambano pamwamba patimu ya Mighty Mukuru Wanderers pomwe akufuna agwiritse ntchito mwayi wosewerera pakhomo.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo pa bwalo la Mpira loweruka mu chikho cha Airtel Top 8 pa masewero achibwereza ndipo wati timu yake yakonzeka kuti ichite bwino.
"Tsopano tili pakhomo tinagonja koyenda nde takonzeka kwambiri ndipo tionetsetsa kuti mwina tidzachite bwino chifukwa tili pakwathu nde tigwira ntchito mwayi wapakhomo." Anatero Kajawa.
Iye wati anyamata onse alibwino pomwe palibe wavulala ndipo chomwe apitilire pabwalo la Mpira ndi kukayesetsa kuti akagonjetse Manoma.
Timuyi ikuchokera kopambana masewero awiri ndi FCB Nyasa Big Bullets komanso Baka City ndipo inagonja 1-0 mmasewero oyamba ndi Wanderers yomweyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores