"MAPENATE NDI LOTALE BASI" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Trevor Kajawa, wati ndi okondwa ndi mmene osewera ake achitira mu mphindi 90 za masewero awo ndi Mighty Mukuru Wanderers ndipo kugonja mmapenate ndi zoti aliyense amakhala ndi mwayi basi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 4-2 pa mapenate kutsatira kupambana 1-0 mu mphindi 90 kuti athere 1-1 pa masewero abwino ndipo Kajawa wati kakonzedwe kawo kanayenda bwino.
"Anali masewero abwino tapambana mu mphindi 90 koma mapenate ndi lotale tagonja koma ndiwayamikire anyamata anga poti agwira ntchito yotamandika kwambiri." Anatero Kajawa.
Iye wati ndi mmene timuyi yachitira mmasewero omwe watsogolera, zikupereka chilimbikitso kuti mu ligi akhale akuchita bwino ndipo atha osatulukanso mu ligiyi.
Timuyi tsopano yatuluka mu chikho cha Airtel Top 8 chomwe amasewera koyamba ndipo masewero awo otsatira aliko lachitatu pomwe akumane ndi Silver Strikers.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores