"TIGWIRA NDI MPONDA NGATI TINACHITA NDI PASUWA" - SINGO
Katswiri wosewera pakati kutimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Yankho Singo, wati iye asewera chimodzimodzi pansi pa mphunzitsi watsopano, Peter Mponda, chimodzimodzi mmene ankasewerera ndi Kalisto Pasuwa kamba koti akusewerera timu.
Iye amayankhula atatha kusaina mgwirizano wa zaka zitatu zoonjezera ndi timuyi ndipo wati ndi wokondwa kukhalabe kutimu yaikulu ngati Bullets.
Iye wati akuyembekeza kuchitabe bwino ndi timuyi ndipo alimbikira kuti akhalebe wodalilika kutimuyi ndikusewera mozipereka.
"Mphunzitsi aliyense tikuyenera kugwira naye ntchito chimodzimodzi nde a Mponda tilimbikira ngati timachitira mmbuyo muja palibe kusiyana ayi. Ngati osewera, umayenera kulimbikira pa mphunzitsi aliyense." Anatero Singo.
Osewerayu anachokera kutimu yachisodzera ya Bullets mu 2022 ndipo mu zakazi wazitolera Kwambiri mpaka wasewerako timu ya dziko lino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores