Jika: Bangwe muyionanso ikumenya mpira
Mwini wake watimu ya Bangwe All Stars, Mphatso Jika, wati chitsogolo chenicheni cha timuyi sichinaoneke poti akudikilira mkumano ndi anthu osiyanasiyana omwe amakhudzidwa ndi timuyi koma wapereka chilimbikitso kuti timuyi ikadalipo.
Iye amayankhula kutsatira mphekesera zomwe zikumamveka kuti atha kuyisiya timuyi kutsatira kutuluka mu ligi yaikulu ya TNM mu chaka cha 2024.
Iye wati ndi wodandaula kwambiri kamba koti khumbo lake loti timuyi ikhale imodzi mwa matimu akuluakulu linathera panjira komabe timuyi ipitilirabe ndipo banja lake linavomereza.
" A CEO athu anachokapo anapita ku China koma afika pompano tikatero nde tidzakambirana zonse zokhudza timu chifukwa ndi anthu oti atithandiza kwambiri nde chiganizo sindingapange ndekha." Anatero.
Bangwe All Stars inalowa mu ligi mu chaka cha 2023 pomwe inamaliza pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7) koma mu chaka cha 2024 inakanika kutsalabe pa tsiku lomaliza itagonja 1-4 ndi Creck Sporting Club.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores