KUSINTHA KWA NDONDOMEKO YA MPIKISANO WOLOSERA PA OWINNA.
Tikulengeza za kusintha kwa mpikisano wosolera pa Owinna mnjira zitatu motere:
1. Olandira mphoto akhala omwe afika kapena kudutsa pa nambala 4 pa mndandanda wa olosera molondola, kusiyana ndi mmbuyomu pomwe amalandira ndi omwe afika kapena kudutsa pa nambala 2. Izi ziyambira amene apambane sabata ino omwe adziwike Lolemba pa 17 Feb 2025.
2. Mphoto imene olosera molondola amagawana sabata iliyonse ikwera kuchoka pa MK30,000 kufika pa MK40,000. Izinso ziyambira omwe apambane sabata ino.
3. Usiku walero, tiyamba kubisa zigoli zomwe ena alosera gemu isanayambe. Olosera adziona zigoli zawo zokha pomwe za ena idzingolemba "Prediction *-*" basi. Tidzionetsanso momwe anthu ambiri aloserera poonetsa nambala yanthu omwe aloserera mofanana.
Zabwino zonse pamene tikupitiriza kunyadira akatswiri odziwa kulosera!
Komano bola pasayende chinyengo Maka pomabisa prediction zawenazo. Komabe tanyadila kwambili powonjezela ndalamazo.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores