Demakude: Chimwemwe changa ndi chachikulu
Katswiri yemwe wasaina mgwirizano wake ndi Silver Strikers, Felix Demakude, wati akuyembekezera kuti kaseweredwe kake kasintha kwambiri poti akumana ndi osewera ena omwe amuthandizenso kwambiri.
Iye amayankhula atasaina mgwirizano wa zaka zitatu ndi timuyi pomwe wapitako mwaulere ndipo wati ndi okondwa popita imodzi mwa matimu akuluakulu mdziko muno.
Iye anati: "Ndikukhulupilira kuti kaseweredwe kanga kasintha chifukwa kulinso anzanga omwe amapita ku Flames nde tikhale tikuthandizana kupititsa timu patsogolo." Iye anafotokoza.
Demakude amasewera timu ya Bangwe All Stars chaka chatha koma waphunzira kwambiri mpira wake ku FCB Nyasa Big Bullets Reserve.
Iye wakhala osewera wachitatu kusaina ndi timu ya Silver Strikers chaka chino pomwe yasainako Sam Adeyemi komanso Festus Duwe.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores