Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
MPOKERA: "OSEWERA ALIYENSE AMAFUNA ATASEWERAKO BULLETS"
Wosewera watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Blessings Mpokera, wati ndi zinthu zokoma Kwambiri kusaina mgwirizano woonjezera kutimuyi poti ndi zopambana kukhala ku timu yaikulu ngati Bullets.
Iye amayankhula atasaina mgwirizano wa zaka ziwiri kupitilira kukhalabe kutimuyi kufika mu chaka cha 2027 ndipo wati akuyembekezeka kuti akhale ndi nthawi yabwino kutimuyi.
Iye wati chaka chatha timuyi sinachite bwino pomwe inavutika kwambiri koma chaka chino osewera ayesetsa kuti zinthu zikhale bwino ndipo savutika pansi pa mphunzitsi watsopano, Peter Mponda.
"Ndikukhulupilira kuti pomwe a Mponda anali ndi Pasuwa anaphunzira zambiri nde sitiona kusiyana poti mpira wawo ndi umodzi."
Mpokera ndi mmodzi mwa osewera omwe anachokera kutimu yachisodzera yatimuyi ndipo amasewera pakati komanso kumbuyo kwa timuyi.