"MASEWERO AKADALI AMBIRI TIDIKIRE" - MPONDA
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter Mponda, wati masewero akadalipo ambiri ndipo anthu adikirebe pa nkhani yoti tsopano ligi ili mmanja mwawo kuti ayitaye.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa timu ya FCB Nyasa Big Bullets 1-0 pa bwalo la Kamuzu ndipo anati ntchito ikadalipo kuti atenge chikho cha chaka chino.
"Sitinganeneretu kuti titenga ligi chifukwa masewero akadalipobe ambiri, tasewera 9 ndipo atsala ena ambiri nde Ife tikutenga mmene masewero aliwonse alili, tingolimbikira kuti mwina ziyende bwino." Anatero Mponda.
Iye wati timu yake inasewera bwino mmasewerowa pomwe inakwanitsa kupeza mipata yambiri koma inakanika kugoletsa ndipo wathokoza Chinsisi Maonga kamba ka chigoli chake.
Timu ya Silver Strikers tsopano ili ndi mapointsi 25 pa masewero asanu ndi anayi (9) pamwamba pa ligi pomwe apambana kasanu ndi katatu (8) ndi kufanana mphamvu kamodzi.