Login with Facebook to post predictions, updates & live scores
"AYI! AYI! SITINAGULITSE MASEWERO" - MKANDAWIRE
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Red Lions, Malumbo Mkandawire, wati timu yake inavutika kwambiri kamba koti Moyale inawapanikiza kwambiri makamaka mchigawo chachiwiri.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 7-0 pa bwalo la Mzuzu ndipo wati timu yake sinagulitseko masewerowa koma kungoti zawavuta basi.
"Masewero sanali abwino poti sitinasewere bwino komanso kuti Moyale inatipanikiza kwambiri nde zinapangitsa kuti atichinye zigoli zambiri. Ayi ayi sikuti chifukwa choti tonse ndi asilikali ayi koma anzathuwa anatipanikiza kwambiri nde tikaphwasulanso timuyi ndi kukonzanso." Anatero Mkandawire.
Red Lions imapita mmasewerowa ikudziwika kale kuti yatuluka ndipo mchigawo choyamba imatsalira 1-0 ndipo zisanu ndi chimodzi zinazo zabwera mchigawo chachiwiri. Timuyi yamaliza ndi mapointsi 29 pa masewero 30.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
RED LIONS YATULUKA MU SUPA LIGI
Timu ya Red Lions ikubwereranso ku ligi yaying'ono yakummwera kwa dziko lino ya Thumbs Up Southern Region Football league pomwe yatuluka muligiyi loweruka angakhale kuti sinasewere masewero kamba koti MAFCO yatola pointi lero.
Lions inali ndi 29 points ndipo pamafunikira kuti adzagonjetse Moyale Barracks ndi zigoli zodutsa 13 komanso kuti MAFCO isatole pointi iliyonse koma maloto amenewo akanika.
MAFCO yatola pointi imodzi kuti ifike pa mapointsi 33 chimodzimodzi Ekwendeni Hammers komanso Civo United yomwe Red Lions singafikire kuti itsatire Extreme FC kotuluka. Awa ndi matimu ena omwe ali pa chiopsezo chotuluka.
8. Dedza Dynamos 28 -8 35 9. Blue Eagles 28 1 34 10. Mighty Tigers 27 -2 34 11. Civo United 28 0 33 12. MAFCO 28 -8 33 13. Ekwendeni Hammers 29 -12 33 14. Moyale Barracks 28 -7 31
Reported by Hastings Wadza Kasonga Jr
RED LIONS IKUFUNIKIRA ZIGOLI 13 KUTI ITSALE MU LIGI
Moyo wa timu ya Red Lions kuti isatuluke mu ligi ya TNM ya chaka chino ukunka nucheperabe pomwe tsopano ikufunikira zigoli 13 kuti idzapambane pomwe idzakumane ndi Moyale Barracks mmasewero omaliza.
Timuyi yalepherana 1-1 ndi FCB Nyasa Big Bullets pa bwalo la Balaka ndipo kupambana kwa Ekwendeni Hammers pa Civo United 3-2 kwaononga moyo wawo pomwe maso awo akuyang'ana pa MAFCO yomwe ili pa nambala 13 ndi 32 points.
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimuyi, Chifundo Masapula, yemwe nthawiyi samadziwa zotsatira za masewero ena, anati ngati moyo ulipobe, akalimbikira posewera ndi Moyale.
"Sitikudziwa kuti mmene anzathu asewera kuti zili bwanji komabe ngati agonja ndekuti ndi Moyale tidzapita ndi mphamvu zonse kuti tidzachite bwino." Anatero Masapula.
Lions ili ndi mapointsi 29 pa masewero 29 omwe yasewera mu ligiyi ndipo ikadali pa nambala 15 mu ligiyi.
"TIKHONZA KUTSALIRABE MU LIGI" - MASAPULA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Red Lions, Chifundo Masapula, wati timu yake tsopano ili ndi mwayi oti itha kutsala mu ligi pomwe tsopano akufunikira kuchita bwino mmasewero awo.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe timuyi yagonjetsa Extreme FC 2-1 pa bwalo la Balaka ndipo wati mmene anyamata ake akuchitira, akupereka chilimbikitso kuti atsala mu ligi.
"Kukonzekera kwathu kunali kwa pamwamba chifukwa timadziwa kuti masewero alero ndi apampeni koma tithokoze kuti tawina. Mwayi ulipo wochuluka, anyamata akuonetsa kuti ali tsopano bwino koma asamasuke kuti alibwino chifukwa zikhonza kuwasokonekera." Anatero Masapula.
Timuyi ili pa nambala 15 mu ligi ndipo yatsala ndi masewero okwana atatu kuti imalize ligi ndipo ikufunikira mapointsi anayi kuti ichoke ku chigwa cha matimu otuluka ndipo ili ndi mapointsi 25.
"MWAYI UKADALIPO OTSALA MU LIGI" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watimu ya Red Lions, Malumbo Mkandawire, wati timu yake iyesetsabe kumenyera nkhondo mmasewero omwe atsala nawo kuti mwina asatuluke mu ligi pomwe wati mwayi akadali nawo.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe afanana mphamvu ndi Civo United 0-0 pa bwalo la Civo ndipo wati ndi wokhutira ndi zotsatirazi zomwe zithandize timu yawo.
"Poti tinali koyenda, point ndi yabwino ndipo ndasangalala nayo pomwe sitinagonje. Mwayi ukadalipo ndipo tikhala tikuyesabe kuti mwina tisatuluke koma mwayi ulipobe." Anatero Mkandawire.
Red Lions yatsala ndi masewero anayi ndipo akuyenera kupambana mmasewero onse kuti mwina angatsale mu ligiyi pomwe ali ndi mapointsi 22 pa masewero 26 pa nambala 15.
#KasongaJr
"SITIKUYIMIKA MANJA MMWAMBA MONGA RED LIONS" - MASAPULA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Red Lions, Chifundo Masapula, wati timu ya Red Lions iyesabe mmasewero awo omwe atsala kuti imenyere nkhondo yosatuluka mu ligi pomwe wati iwo sanatuluke.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 2-0 pa bwalo la Balaka ndi Kamuzu Barracks ndipo wati kuchinyitsa mwachangu ndi komwe kunawapweteketsa koma ayesetsa mmasewero omwe yatsala nawo.
"Tivomereze kuti tatayadi mapointsi, sitinasewere monga mwa plan yathu mwina zigoli tinachinyitsa koyambilira zinatibalalitsa tivomereze kuti taluza. Masewero akadalipo, sitikufooka mmasewero omwe atsalawo tiyesetsa kuti tiwine." Anatero Masapula.
Timu ya Red Lions yatsakamira pa nambala 15 pomwe ili ndi mapointsi 21 pa masewero okwana 25 omwe yasewera mu ligi ya TNM.
#Tawonga2023
"RED LIONS SITULUKA MU LIGIYI" - MASAPULA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Red Lions, Chifundo Masapula, wati chipambano chomwe apeza ku Karonga lachitatu ndi chokoma kwambiri ndipo chawalimbitsa mtima kuti satuluka mu ligi ya chaka chino.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe yagonjetsa Karonga United 3-2 pomwe inamwetsa zigoli zitatu mu mphindi zisanu zakumapeto kuti apeze chipambanochi. Iye watsindika kuti sakutuluka.
"Tithokoze anyamata kuti anaikirapo mtima ndipo ena omwe anachokera panja sanataye mtima, mutha kuona anzathu anapeza zigoli zawo komabe ife tiwalimbirabe. Red Lions chaka chino sikutuluka, apa tafika 21 tikapambana Ina tikhala tikusunthabe." Anatero Masapula.
Chipambanochi changosintha mapointsi pomwe tsopano ili ndi 21 pa masewero 24 omwe yasewera chaka chino koma ikadalibe pa nambala 15 mu ligiyi.
"KACHEZENI NDI OYIMBIRA OSATI IFE" - RED LIONS
Aphunzitsi a timu ya Red Lions anakana kuyankhula ndi olemba nkhani a mdziko muno atatha masewero ndipo anawauza kuti akacheze ndi oyimbira poti ndi omwe apambana masewerowa.
Izi zinachitika kutsatira kugonja kwa timuyi ndi Chitipa United 1-0 pomwe eni khomowa anapatsidwa penate pa mphindi 88 za masewerowa yomwe Ramadhan Ntafu anagoletsa.
Atolankhani atapita kuti ayankhulane nawo anati apite kwa oyimbira poti ndi amene apambana masewerowa ndipo iwo sakufuna.
Timu ya Red Lions ili pa nambala yachikhumi ndi chisanu (15) pomwe yatolera mapointsi 18 pa masewero 23 omwe yasewera.
"NZOTHEKA RED LIONS OSATULUKA MU LIGI" - MASAPULA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Red Lions, Chifundo Masapula watsimikiza kuti ndi zotheka kuti timu yake isatuluke mu ligi koma zitengera mmene anyamata ake aziperekere mmasewero omwe atsala nawo.
Masapula amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 2-0 ndi timu ya Blue Eagles pa bwalo la Balaka ndipo wauza Sports Torch kuti timuyi ikungofunikira zipambano zingapo kuti ichoke kumunsi komwe iwo ali.
"Tikamasewera masewero timakhala ndi cholinga chimodzi, kuti tipambane masewerowa koma apa zikuvuta tagonja, tiyesetsa mmasewero atsalawa ndi ochepa koma titapambanako 4 kapena 5 mwina titha kuchoka kumunsi, sitingapeze osewera ena kuti asewere panopa, ndi omwewa nde tingowalimbikitsa kuti aike mtima." Anatero Masapula.
Red Lions yatsala ndi masewero okwana asanu ndi atatu (8) ndipo yatsakamirabe pa nambala yachikhumi ndi chisanu (15) pomwe yatolera mapointsi 18.
"MASEWERO ATSALA ANGAPO, TIYAMBA KUCHITA BWINO" - NDAWA
Mphunzitsi watimu ya Red Lions, Franco Ndawa, wati ochemerera atimuyi asataye mtima kuti mwina timuyi ituluka pomwe wati kwatsalabe masewero omwe atha kuwapulumutsa mu ligi.
Ndawa amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 2-0 pakhomo ndi Bangwe All Stars ndipo wati timu yake imaphonya kwambiri mipata yochuluka komabe ayesetsa kuzitolera kutsogoloku.
"Tinayesetsa kukonza mavuto athu osagoletsa koma kubwera mmasewerowa taphonya kwambiri kenako tayamba kuchinyitsa. Zinthu zikuvuta tivomereze koma masewero alipo angapo ngakhale akupita komabe tiyesetsa kuchita bwino mmasewero enawa." Anatero Ndawa.
Timu ya Red Lions ikufunika mapointsi okwana asanu ndi imodzi (6) kuti ituluke mu chigwa cha matimu osatuluka mu ligi pomwe ili ndi mapointsi 18 pa masewero 21 omwe yasewera.
"MASEWERO AKADALIPOBE NDIPO TIYESETSA" - MKANDAWIRE
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Red Lions, Malumbo Mkandawire, wati timu yake iyesetsa kulimbikira mmasewero khumi omwe atsala nawo kuti amalize ligi ya chaka chino ndi cholinga choti achoke kumunsi kwa ligiyi.
Mkandawire amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 1-0 ndi Mighty Wakawaka Tigers pa bwalo la Kamuzu ndipo anati timu yake yaphonya mipata yochuluka. Iye wati ayesetsa mmasewero omwe atsala nawo kuti asatuluke mu ligi.
"Apapa zinthu zikuipadi komabe tidikire chifukwa masewero atsala angapo, ife tatsala ndi 10 nde tiyesetsa kuwauza anyamata kuti alimbikire ndi cholinga choti tichoke kumunsi komwe tiliko." Anatero Mkandawire.
Lions yatsakamira pa nambala 15 pomwe yakwanitsa kupeza mapointsi 18 pa masewero 20 omwe asewera mu ligi ya TNM.
"TIKUONONGA NDALAMA POMWE OYIMBIRA AKUONONGABE ZINTHU" - MAPASULA
Mmodzi mwa akuluakulu ophunzitsa timu ya Red Lions, Chifundo Mapasula, wadandaula ndi oyimbira yemwe anali pa masewero awo ndi timu ya Dedza Dynamos ponena kuti watengapo mbali kuti timu yake igonje mmasewerowa.
Iye amayankhula izi atatha masewero awo omwe agonja 2-0 ndi timu ya Dedza Dynamos ndipo wati mchitidwe wa oyimbira ukusokoneza matimu ambiri mdziko muno.
"Oyimbira watengapo mbali sinali penate, osewera uja mpira unamumenya pa phewa koma apereka penate zomwe zikuchitikazi akutipondereza kwambiri chifukwa tikugwiritsa ntchito ndalama tikamasewera mpirawu koma oyimbira akumakhala ndi matimu nde nzosokoneza." Anatero Mapasula.
Iye anati timuyi inalinso ndi mavuto ena ochepa omwe akonze patsogolo pa masewero awo otsatira. Lions ili pa nambala 15 pomwe ili ndi mapointsi 18 pa masewero 18.
Red Lions has fired head coach, Mike Kumanga and has replaced him with former Civo United mentor, Franco Ndawa.
Lions sits 15th on the table with 4 points from 8 games.
go ma reds
Referees to shun Red Lions game against Moyale Barracks on Saturday if Super League of Malawi (Sulom) fails to take disciplinary action against the team.
It is reported that some players manhandled National Football Referees Association treasurer.
Red Lions to miss coach Kumanga: Alick Chirwa stand-in Red Lions head coach Mike Kumanga will not be available for the Zomba-based side a considerable period of time to continue taking charge of... www.nyasatimes.com
Timu ya Red Lions yati Chikoti Chirwa asewelera timuyi chaka chino.
Malingana ndi timuyi, osewerayu anapita ku timu ya Kamuzu Barracks kaamba koti timuyi inatuluka mu ligi yaikulu ya mdziko muno.
Kumanga back at Red Lions as head coach Zomba-based military outfit, Red Lions, has announced the return of Mike Kumanga at the club www.nyasatimes.com
13 players have successfully joined Red Lions ahead of 2020 football season.
The Zomba based team has confirmed the development.